Friday, August 15, 2025
No menu items!
spot_img
HomePoliticsTipeleke Mwayi wina  kwa Mai Banda kuti umoyo wa anthu usinthe"* -...

Tipeleke Mwayi wina  kwa Mai Banda kuti umoyo wa anthu usinthe”* – Mwandira

Wolemba: Andrew Tembo

Chipani cha Peoples(PP) chamemeza anthu kuti adzavotele mtsogoleri wawo Mai Joyce Banda yemwe adalamulira dzikoli kwa zaka ziwiri zokha kuti tsopano adzapitilize ntchito zake za chitukuko maka pa nkhani ya kupeleka mwayi kwa anthu kuchita ulimi wa ziweto ndi bizinesi za mayendedwe.

Gavanala wa chipanichi Ku dera la Mbayani ,Chemusa Magasa mu mzindawu Watson Mwandira ndiye wayankhula izi pamsokhano  wokonzekeletsa anthu za kubwera kwa mtsogoleri wa chipanichi loweluka likudzali yemwe akuyembezereka kudzacheleza anthu Ku Ndirande pa bwalo la za masewelo la Nyambadwe.



Iye wati mu mbiri ya dziko lino ,Mai Joyce Banda ndi mtsogoleri yemwe anayambitsa Kabaza wa njinga (zamoto ndi za kapalasa) komanso kulimbikitsa ulimi wa mbuzi ndi ng’ombe popeleka kwa ulele kwa anthu m’dziko muno.

“Tiyeni loweluka likubwereri tikawalandire Mai Joyce Banda ,mtsogoleri wathu ,yemwe mu nthawi yake yochepa anakwanitsa kusitha miyo ya anthu popeleka zochita monga ulimi wa ziweto ndi kuyambitsa anthu kuchita matola a njinga,ttiwavotele kuti adzapitilize izi” anatelo a Mwandira.

Chipani cha Peoples  ndi chimodzi mwa zipani zomwe ndi zodziwika bwino m’dziko lino ndipo mtsogoleri wake analamulira dziko kwa zaka ziwiri potsatira infa ya mtsogoleri wakale Bingu wa Muntharika yemwe anali wachitatu chiyambireni pomwe dziko lino linachoka mu ulamuliro wa a zungu(atsamunda).

RELATED ARTICLES
- Advertisment -
Google search engine

Most Popular

Recent Comments