Saturday, April 18, 2026
No menu items!
spot_img
HomeNationalKamangila wati Prince Barber amagulitsa mankhwala ozunguza bongo

Kamangila wati Prince Barber amagulitsa mankhwala ozunguza bongo



Wolemba: Mtolankhani Wathu

Loya Alexious Kamangila wati Prince Butani yemwe ali ndi malo ometeramo tsitsi apamwamba mumzinda wa Lilongwe komaso Blanytre amachita malonda ogulitsa mankhwala ozunguza bongo komaso kuzembetsa chuma chadziko lino.

Kamangila wane izi kudzera patsamba lake la mchezo la Facebook.

“BARBER 1 is into drug business & Money-Laundering. Norman Paulosi Chisale must know this,” watelo Kamangila.



“Prince Barbershops- Malawi, if you bought a 200mil car, it means you earned 200ml meaning you paid a minimum of 60mil in Tax. Share your Tax returns. Nkhani tiyambe,” waonjezera motero Kamangila.

Zonsezi zikudza patatha tsiku Butani atayika zithuzi za galimoto ya mtundu wa Ford Wildtrack yomwe mtengo wake ndiwapakati pa K200 million komaso K400 million.

Aka sikoyamba Butani kugula galimoto za mitengo yapamwamba yotele zomwe nthawi zambiri zimadzetsa manong’onong’o pakati pa anthu ngati ndalama zochitira izi zimachokadi mu bizinesi yake yometa tsitsi.

Pakadali pano ometa odziwika bwinoyi sanadayankhulepo kalikonse pankhaniyi.

RELATED ARTICLES
- Advertisment -
Google search engine

Most Popular

Recent Comments