Wolemba: Mtolankhani wathu
Anthu ochuluka patsamba la mchezo la Facebook adzudzula Mtsogoleri wachipani cha AFORD a Enoch Chihana ati kamba konamizira kuti achitidwa chipongwe pomwe nkhaniyi ndiyochita kukonza ngati sewero.
Anthu omwe anayika ndemanga zawo pa tsamba la pa Facebook la Malawi Voice anati zomwe otsatira a Chihana akunena kuti zawachitikira ku Kasungu si chiwembu koma sewero lomwe anakonza pofuna kuyipitsa mbiri yachipani cholamula cha MCP.

Mu kanema yemwe akuyenda pa masamba a mchezo munthu wina akufotokoza kuti anthu ovala makaka achipani cha MCP omwe amayendera galimoto lomwe nambala yake ndi KU 2 C, amafuna kupha a Chihana pomwe amachokera ku msonkhano m’bomalo.
Koma anthu omwe ayika ndemanga zawo pankhaniyi adzudzula a Chihana ponena kuti anachita kukonza zomwe zinachitikazo pofuna kuti anthu awamvere chisoni.
Izi ndi zina mwa ndemanga zomwe anthu alemba pankhaniyi
Happy Karamazov Chatha
“Sounds and seems scripted”
Lawrence Ndekha
“Chihana and Kamlepo same band wagon.”
Gibson Nachiye
“Chihana Drama Group. Only fools can believe this.”
Paul Kagona
“How can the attackers clad in MCP attire? Sounds like it’s an inside stunt. To beg sympathy from people and to mudsling the MCP. Whatever that sympathy won’t reach Chihana and his DPP cadres.
Lazarus Chalumako Moto
“Ochita chipongwe dressed up in party attire. Sounds fishy.
Stain wa Douglas
“DPP never again. This stupid propaganda must stop at all cost. Malawians are looking for development. Opposition youma mitu ngati iyi simunayione mkale lonse.”
