Wolemba: Mtolankhani wathu
Yemwe akuyima ngati wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino komanso wa chipani cha Malawi Congress (MCP) pachisankho cha pa 16 September, a Vitumbiko Mumba, akonza misonkhano yoyimaima mchigawo cha kumpoto komwe akuyembekezeka kukafotokozera anthu mfundo zachitukuko zomwe chipanichi chakonza.
Misonkhanoyi ikuyamba lachitatu pa 20 September pomwe a Mumba akafike ku Chitimba m’boma la Rumphi komanso ku Khwawa, Mlare ndi Luchali m’boma la Karonga.

Lachinayi a Mumba akachititsa misonkhano ku Nkhwangwa komwe ndi kumpoto kwa boma la Chitipa, Ifumbo komwe ndi pakati pa boma la Chitipa komanso ku Wililo m’boma la Karonga.
Lachisanu pa 22 September a Mumba akafika ku Songwe, Ngelenge Lufilya, Kambwe komanso ku Baka m’boma la Karonga.
M’malo onsewa a Mumba akakhala ndi olemekezeka a Kezzie Msukwa, a Uchizi Mkandawire, a Leonard Mwalwanda, Job Msowoya, Kuseka Nyasulu, a Adam Beza,a Isaiah Mhango ndi akuluakulu ena.