Wolemba: Durrell Namasani
Katswiri woyimba Gibo Pearson watulutsa nyimbo ina yatsopano yotchedwa “Ndidzabwenzanji” yomwe ikusonyeza kuti igwedeza kwambiri m’malo ambiri m’masiku akudzawa.
Giboh, yemwe dzina lake lenileni ndi Gift Pearson, watulutsa nyimboyi m’mawa wa lachisanu ndipo anthu ochuluka ayamba kale kuyamikira.

Mu nyimboyi, munthu akuyamikira wachikondi wake kamba kachikondi chomwe amapereka ndipo akulonjeza kuti sadzamusiya ngakhale anthu atakamba zoyipa za wachikondiyo.
“ndipite pa guwa ..ndikachitire umboni mmene amandikondera….
ndipite pa Radio .. ndikangolengeza mmene amandikondera…
Ndidzabwenzanji kwa alamwanu ×4″ , ikumatero nyimboyo pa Chorus.
Nyimboyi yajambulidwa ndi Pearson pomwe kanema wake yemwe akuwonekanso owala bwino wajambulidwa ndi katswiri wodziwika bwino pojambula nyimbo Twice P.
Mukhoza kuwonera kanema watsopano wa Gibo Pearson potsatira link yomwe ili m’musimu.
