Wolemba: Mtolankhani wathu
Wachiwiri kwa President Lazarus Chakwera pachisankho cha pa 16 September, a Vitumbiko Mumba alimbikitsa anthu apa zilumba za Likoma ndi Chizumulu kupitilira kukhala pambuyo pa President Chakwera pakuti ndiyekhayo yemwe ali ndi masomphenya wotukula zilumbazi.
A Mumba omwenso ndi nduna ya zamalonda ndi mafakitale apereka pempholi lachisanu pomwe anayenda ulendo wa pa madzi kukacheza ndi anthu apa zilumbazi.
A Mumba ati President Chakwera ndiwokonzeka kutukula maderawa komanso ntchito za maulendo apa nyanja zomwe maboma ena ammbuyomu samaziyikira pamtima.

Pamenepa a Mumba ati anthu apa zilumbazi omwe analembetsa mkaundula wazisankho, akuyenera kuvotera a Chakwera lachiwiri sabata ya mawa ndipo kuti asapusitsike ndi atsogoleri ena adyera omwe akungofuna kuwagwiritsa ntchito kuti apeze mavoti
Pa ulendowu a Mumba anaperekezedwa ndi mkulu wa achinyamata mchipani cha MCP a Baba Steven Malondera ndi akuluakulu ena.
Chipani cholamula cha Malawi Congress ndichomwe chikuoneka kuti chiri ndi chikoka pa zilumbazi potengera unyinji wa anthu omwe wakhala ukusonkhana m’misonkhano yachipanichi.


