Wolemba: Durrell Namasani
Wachiwiri kwa Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera pachisankho cha pa 16 September a Vitumbiko Mumba ati chipani cha DPP ndiro gwero la mavuto omwe anthu mdziko muno akukumana nawo.
A Mumba alankhula izi ku Mzuzu pa misonkhano yomaliza yokopa anthu pomwe patsala masiku awiri tsopano kuti chisankhochi chichitike.

A Mumba ati chipani cha DPP chinasokoneza zinthu zambiri m’boma chifukwa cha kuba komanso katangale.
Iwo ati izi ndizomwe zinachititsa kuti ulamuliro omwe ulipo pano wa Dr Chakwera ukumane ndi mavuto ochuluka monga kusowa kwa ndalama za kunja ndi zina.
Komabe a Mumba ati a Chakwera kudzera kuchipani cha Malawi Congress (MCP) ayesetsa kukonza zinthu zina ndipo posachedwa akhale akuthana ndi mavuto onse omwe boma lakale la DPP linabweretsa.
Iwo atinso mkulakwa kuti lero chipani cha DPP chidziwuza anthu kuti chiri ndikuthekera kothetsa mavuto omwe ali mdziko muno.
Pamenepa a Mumba apempha anthu kuti asanamizidwe ndi bodza lomwe chipani cha DPP chikulonjeza kamba koti chikungofuna kubwereranso m’boma kuti chikapitirize kuba osati kutumikira a Malawi.