Wednesday, July 2, 2025
No menu items!
spot_img
HomeEntertainmentNjobvu Ziwiri Za Ku Balaka' zifotokoza zakusiyana kwawo

Njobvu Ziwiri Za Ku Balaka’ zifotokoza zakusiyana kwawo

Wolemba: McLloyd Kudzingo


Oyimba odziwika bwino mdziko muno Paul Subili ndi Rod Valamanja omwe amkadziwika kuti ‘Njobvu Ziwiri Za Ku Balaka’ ati kuchuluka kwa udindo ndikusintha kwa anthu otsatira nyimbo ndi zina zomwe zinachititsa kuti awiriwa asamayimbirenso limodzi.

Iwo ati kuchokera mchaka cha 1999 pomwe iwo adayamba kuyimbira limodzi, zinthu zakhala zikusintha kufikira mchaka cha 2005 pomwe awiriwa anaganiza zomachita zinthu zina zowonjezera.

Iwo ati izi zinachitika kamba koti ndalama imene amapeza kudzera mu kuyimba siyimakwanira kusamalira iwo ndi maanja awo.

Rod Valamanja ndi Paul Subiri



Malinga ndi uthenga wa patsamba la mchezo womwe Subili walemba, iye adakali mdziko muno komwe mwazina amayimba ndi gulu la Alleluya  pomwe  Rod Valamanja ali mdziko la South Africa komwe akugwirakonso ntchito kupatula kuyimba.

“Poti kuyimba kuli ngati ufiti, mchifukwa chake Valamanja akumatulutsa nyimbo ndi oyimba ena koma sizikutanthauza kuti tinadana ayi. Inenso ndimayimba ndi ena ndipo sizikutanthauza kuti ndadana ndi Valamanja. Valamanja ali ku South Africa, Paul Subili ndili kuno ku Malawi kuthamanga kuti ana asatupe. Sitikuyinyoza music  koma panopa monga azibambo a maudindo tidayamba kuthamanganso zina,” anatero Subili.

Subili watinso anthu omwe amkafika ku malo azisangalalo komwe oyimbawa amkayimba, pano anasiya kupita ku malo-wa ndipo m’malo mwake amangomvera nyimbo za oyimbawa kunyumba.

Iye waonjezeranso kuti achinyamata a lero samatsata kwenikweni nyimbo za kale chifukwa masiku ano oyimba achuluka zomwe zikuchititsa kuti oyimba akale asamakhale ndi chikoka kwenikweni.

Komabe Subiri wathokoza anthu omwe akhala akutsata nyimbo zawo kuyambira pomwe adayamba kuyimba mpakana pano ndipo alonjeza kuti awiri azikhalabe akuyimba pawokhapawokha mipata ikamapezeka.

Subili ndi Valamanja anadziwika kwambiri mu chaka cha 1999 atatulutsa chimbale cha ‘Tigwire Mtengo Wanji’ ndipo ayimbakonso nyimbo zina zotchuka ngati Taononga Dziko , Anali ndi Cholinga, Ndiwe Mbambande komanso Kilini Ya Mkwati.

Mukhoza kuwonera zina mwa nyimbo zomwe awiriwa anayimbira limodzi potsatira link Ili m’musiyi
https://youtu.be/tSV_Gh3f2FY?si=TsT_dkfyTtTVHXZ-

RELATED ARTICLES
- Advertisment -
Google search engine

Most Popular

Recent Comments