Wolemba: Durrell Namasani
Wachiwiri kwa President Lazarus Chakwera pachisankho cha pa 16 September a Vitumbiko Mumba ati chipanichi sichikufuna kulonjeza anthu zosatheka ngati zomwe achipani cha UTM adaabweretsa mu mgwirizano wa Tonse.
Poyankhula ku khwimbi la anthu lomwe linasonkhana ku Kambwe m’boma la Karonga, a Mumba anati malonjezo ena omwe adalonjezedwa ndi Mgwirizano wa Tonse anali ovuta kuwakwaniritsa ndipo mchifukwa chake zinthu zina boma linalephera kuchita.

A Mumba anatchulapo mwachitsanzo nkhani ya feteleza wotsika mtengo yemwe chipani cha UTM chomwe chidalinso mu mgwirizano wa Tonse chidalonjeza a Malawi zomwe sizinakwaniritsidwe.
Iwo anati mu Manifesto ya MCP munalibe nkhani yotsitsa feteleza kufikira pa K4495 ngati m’mene chipani cha UTM chimkakambira.
“2019 mu Manifesto ya MCP munalibe za feteleza wotsika mtengo motero, koma mu Manifesto ya UTM zinalimo. Ine ngati munthu yemwe ndapangapo malonda a feteleza nditamva izi ndidali wodabwitsika kwambiri pakuti zinali zosatheka feteleza kukhala wotchipa chomwechi.”
A Mumba anapitiriza kunena kuti mgwirizano wa Tonse Alliance utayamba pakati pa MCP, UTM ndizipani zina, nkhani ya feteleza ija idakambidwanso ndipo iwo atafunsa a UTM ngati izi zinalidi zotheka anayankhidwa kuti zidzaoneka akalowa m’boma.
A Mumba anati, “Titalowa m’boma tinawafunsanso anzathu a UTM zalonjezo la feteleza wotsika mtengo ndipo anatiyankha kuti lonjezo limene lija zinali ndale chabe pofuna kukopa anthu.”
Pamenepa, a Mumba ati pachisankho cha chaka chino, agwiritsa ntchito mfundo zokhazo zachipani cha Malawi Congress poti ndizomwe ziri zoona powopa kudzaoneka ngati a bodza patsogolo.