Sunday, June 8, 2025
No menu items!
spot_img
HomePoliticsNyamilandu alonjeza kutukula dera la kummwera cha kunzambwe kwa boma la Nsanje

Nyamilandu alonjeza kutukula dera la kummwera cha kunzambwe kwa boma la Nsanje


Wolemba: McLloyd Kudzingo


Yemwe adakhalapo Mtsogoleri wa bungwe lowona za masewero la Football Association of Malawi (FAM) a Walter Nyamilandu Manda ati iwo ndiomwe ali ndi kuthekera kwakukulu kobweretsa zitukukuko zochuluka kudera la kummwera cha kunzambwe kwa boma la Nsanje.

A Nyamilandu amalankhula izi pa bwalo la zamasewero la sukulu ya pulayimale ya Khulubvi  pomwe amachititsa msonkhano wolengeza kuti apikisana nawo pa chisankho cha phungu wa kunyumba ya malamulo waderali.



Iwo ati derali lakhala likumanidwa zitukukuko kwa nthawi yayitali kamba koti mwa zina atsogoleri omwe amasankhidwa kuti atumikire anthu, sayika chidwi pa mfundo yobweretsa zitukukuko yosiyanasiyana kuderali.

Iwo ati akasankhidwa kukhala phungu, awonetsetsa kuti ma kampani a ntchito za malonda monga ma Bank, akuyambitsa ntchito zawo kuderali.

Iwo ati awonetsetsanso kuti bwalo la za masewero la Nsanje lomwe iwo anathandizira kuti limangidwe kuderali, layikidwa malo ochuluka okhalamo anthu.

Iwo ati adzaonetsetsano kuti pa sukulu ya sekondale ya Nsanje pamangidwa nyumba zina zogona ophunzira komanso adzaonetsetsa kuti chipatala chachikulu cha m’bomalo chakonzedwanso.

A Nyamilandu omwe adakhalapo m’modzi mwa akuluakulu ku kampani yopanga sugar ya Illovo, atinso apikisana nawo pa chisankho cha pa 16 September ngati phungu woyima payekha pofuna kuti atumikire anthu mosavuta.

“Mavuto omwe anthu kudera lino akukumana nawo siwokhudza chipani chimodzi chokha koma akukhudza wina aliyense. Ife tikufuna tilankhule chimodzi pakuti tikakhala ogawikana potengera zipani, kukhala kovuta kuti dera lino litukuke,” anatero a Nyamilandu.

Iwo ati nthawi yakwana tsopano yakuti anthu akhale ndi phungu yemwe alidi ndi masomphenya wotukula dera lake.

Pa msonkhanowo panafika khwimbi la anthu lomwe linasangalatsidwanso ndi mayimbidwe agulu loyimba chamba cha Reggae la Ma Blacks.

RELATED ARTICLES
- Advertisment -
Google search engine

Most Popular

Recent Comments