Wolemba Andrew Tembo.
Yemwe akufuna kuimira uphungu wa nyumba ya malamulo mu mzinda wa Blantyre mdera la Chichiri – Misesa ,Mai Illy Majawa Mombera wati iye aonetsetsa kuti anthu ochuluka akhale ndi Mwayi opanga business mdera lake kudzera mu kupeza Mpamba ,akawina mu zisakho za pa 16 September 2025.
Iwo ati ngodya zawo zakhazikiza pa Maso mphenya a dziko a 2063,zomwe Mwa zina ndi kuonetse SA kuti umiyo wa anthu akukhala wabwino,kulimbikitsa Mtendere ,kugwirira ntchito pa modzi ndi kupindura potukuka pa umoyo wa tsiku ndi tsiku ,choncho apempha anthu owalondolo kuti athandize kampeni yawo mwabata ndi Mtendere.

A Mombera alonjeza izi pomwe amapeleka ndi kisindikiza kalata zawo zowayeneretsa kudzapikisana nawo pa mpandowu Ku bungwe loyendetsa zisankho la MEC.
Iwo ati akudziwa bwino kuti mwa ziphyinjo zomwe anthu ambiri akukumana nazo pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku ,ndalama ndi limodzi mwa mavutowa ,choncho Iwo atukula anthuwa mu njirayi.
A Mombera, omwe ndi achipani cha UDF adzapikisana ndi anthu ena asanu omwe ndi azipani za UTM ,DPP,MCP ndi ena awiri omwe ndi oyima pa okha (Independent).
Anthu wa ndi a Eric Chirwa a chipani cha UTM,Enala Shawa a MCP, a Themba Mkandawiire a DPP,Louis Ngalande ndi a Paul Kachitsa omwe ndi oyima pa okha.
Delari linali pansi pa phungu wa DPP a Sameer Sulemani omwe akuyang’anila dera la Chigumula ,BCA, Club Banana,Namiyanga, koma chifukwa cha kusitha kwa malilre komwe a MEC anachita, derali lakhala lopanda phungu kwa zaka ziwiri.
