HomeNewsApolisi agwira anthu awiri pa nkhani ya kupha mtsikana wa zaka 19...

Apolisi agwira anthu awiri pa nkhani ya kupha mtsikana wa zaka 19 ku Mzuzu

Wolemba: Chisomo Phiri

Apolisi mumzinda wa Mzuzu agwira anthu awiri omwe akuwaganizira kuti akukhudzidwa ndi kuphedwa kwa mtsikana wa zaka 19, yemwe thupi lake linapezeka m’mbali mwa msewu wa Zolozolo-Recreation, pafupi ndi bwalo la Mzuzu Upper Stadium pa 24 October 2026.

M’mawu ake, wachiwiri kwa wolankhulira apolisi pa siteshoni ya Mzuzu, Edson Chipeni, watchula anthu omwe agwidwawo kuti ndi Arthur Banda, yemwe amadziwikanso ndi dzina loti Lamboghin, wa zaka 19, wa ku Mzimba, komanso Daniel Dzimbiri, wa zaka 18, wa m’boma la Chiradzulu.

Chipeni wati pa 23 October, cha m’ma 18:00, mtsikanayo anachoka panyumba limodzi ndi mnzake kupita ku konsati ya nyimbo yomwe inkachitikira ku Linde Lounge mumzinda wa Mzuzu, koma sanabwerere kunyumba.

Iye wati tsiku lotsatira, thupi lake linapezeka m’mbali mwa msewu, ndipo kuyezetsa thupi lake pambuyo pa imfayi ku Mzuzu Central Hospital kunasonyeza zizindikiro zosonyeza kuti anachitiridwa nkhanza zogonana

Wayankhula motere Chipeni:“Utapezeka mtembowo, apolisi ofufuza milandu anayamba nthawi yomweyo kufufuza, zomwe zinachititsa kuti anthu omwe akuwaganiziridwawa agwidwe pa 11 November 2026.

“Pa nthawi yofunsidwa mafunso, chibwenzi cha malemuyo komanso mnzake anamuzindikira bwino anthu omwe akuwaganiziridwawa, ponena kuti anali nawo pamodzi pa nthawi imene chochitikacho chinkachitika. Kuphatikiza apo, anthu omwe agwidwawa anavomereza kuti anakangana ndi mboni zonse ziwirizo komanso malemuyo.”

Chipeni wanena kuti kufufuza kukupitirirabe pofuna kugwira anthu ena awiri omwe akuganiziridwa kuti akukhudzidwa ndi mlanduwu ndipo akuthawabe.

RELATED ARTICLES
- Advertisment -
Google search engine

Most Popular

Recent Comments