Wolemba: Chisomo Phiri
Pulofesa David Kamchacha waulula kuti pa mayeso ake a Malawi School Certificate of Education (MSCE) adapeza mapointsi 31, kuphatikizapo giredi 7 pa phunziro la Chingelezi.
Komabe, iye wati zotsatira zake za maphunziro a sekondale sizinakhale cholepheretsa kuti apeze madigiri awiri a PhD komanso kuchita bwino pa ntchito zake m’mayiko osiyanasiyana.

Kamchacha
Malinga ndi wayilesi ya TWR, Pulofesayu wanena izi dzuro pomwe anaonekera pamaso pa komiti ya Nyumba ya Malamulo ngati mtsogoleri wa Association of Private Universities in Malawi (APUMA).
Iye wapempha Nyumba ya Malamulo kuti iwunikenso njira zovomerezera ophunzira m’masukulu a ukachenjede kuti anthu omwe anapeza ma credit asanu pa MSCE nawonso azitha kupitiriza maphunziro apamwamba.
“Chingelezi sichomwe chimasonyeza kuti munthu ndi wanzeru,” watero Kamchacha.
Iye wanenanso kuti anthu ena omwe anapeza ma credit asanu pa MSCE apita patsogolo mpaka kukhala olemba anzawo ntchito komanso kupanga mwayi wa ntchito kwa anthu ena.
Pulofesa Kamchacha ndi m’modzi mwa akatswiri odziwika pa maphunziro apamwamba mdziko muno, zachuma ndi chitukuko, makamaka pankhani za ulimi ndi misika ya zokolola. Iye ndi wochita malonda komanso woyang’anira mabungwe a maphunziro apamwamba.
Ntchito zake zakhala zikukhudza chitukuko cha ulimi, kayendetsedwe ka mabizinesi, ndondomeko za zachuma komanso maphunziro apamwamba kwa zaka zoposa 30.
Iye ali ndi digiri yoyamba ya Bachelor of Business Administration yomwe anaipeza ku Cyprus Institute of Marketing mumzinda wa Nicosia, m’dziko la Cyprus.
Kamchacha anapitiriza maphunziro ake pasukulu yomweyi ndipo anapezanso digiri ya Master of Business Administration (MBA).
Alinso ndi digiri ya PhD mu Strategic Management yomwe anaipeza ku Columbia Commonwealth University.
Katswiriyu alinso ndi PhD ina mu Development Economics and International Development yochokera ku Pebble Hills University.
Pa ziyeneretso zake za ntchito, Kamchacha alinso ndi ziphaso za Fellow of the Chartered Institute of Marketing (FCIM) komanso Member of the Chartered Institute of Marketing (MCIM).
Zochita zake pa maphunziro ndi ntchito zimakhudza zachuma pa ulimi, kayendetsedwe ka mabizinesi, chitukuko cha misika, malonda apadziko lonse komanso ndondomeko za chitukuko.
Ulendo wake wa ntchito unayambira m’makampani asanasamukire ku ntchito zolimbikitsa misika ya zaulimi komanso mapulogalamu a chitukuko cha mayiko.
Pakati pa chaka cha 1983 ndi 1990, anagwira ntchito ku David Whitehead and Sons Limited komanso Blantyre Netting Company ngati kalaliki wowerengera ndalama komanso woyang’anira makompyuta.
Kuyambira mu 1990 mpaka 1992, Kamchacha anagwira ntchito ku Malawi Union of Savings and Credit Cooperatives (MUSCCO) ngati katswiri woyang’anira machitidwe a makompyuta.
Kenako analowa m’kampani ya Norsk Hydro/Farm-Wise, komwe anagwira ntchito ngati Accounting and Operations Manager kuyambira mu 1992 mpaka 1995.
Ntchito zake zinkaphatikizapo kuyang’anira ndalama, kayendetsedwe ka nthambi, kuitanitsa feteleza kuchokera kunja, kayendetsedwe ka mayendedwe komanso kagawidwe ka katundu.
Pambuyo pake, adalowa m’gawo lolimbikitsa misika ya zaulimi ndipo anayamba kugwira ntchito ndi bungwe la International Fertilizer Development Center (IFDC).
Pakati pa 1996 ndi 2000, Kamchacha adagwira nawo ntchito zolimbikitsa misika ya zipangizo zaulimi, makamaka kagawidwe ka feteleza, kumasula malonda komanso kukhazikitsa njira zoyendetsera zipangizo zaulimi.
Pambuyo pake, adagwira ntchito ngati Market Development Specialist ku IFDC, pothandiza kulimbikitsa misika ya feteleza, mbewu komanso mankhwala otetezera mbewu ku tizilombo ndi matenda.
Pakati pa 2003 ndi 2005, Kamchacha anali National Project Director wa pulojekiti ya Sustaining Productive Livelihoods through Inputs for Assets (SPLIFA).
Ntchito zake zinkaphatikizapo kugwirizanitsa kagawidwe ka zipangizo zaulimi, kuthandiza amalonda a zipangizo zaulimi, kuphunzitsa alimi komanso kulimbikitsa mgwirizano pakati pa alimi ndi misika.
Iye adagwiranso ntchito za utsogoleri ku Evangelical Association of Malawi, kuphatikizapo kukhala Chief of Party pa pulogalamu ya dziko lonse yokhudza chitetezo cha chakudya komanso kuchepetsa mavuto obwera chifukwa cha masoka.


