Wolemba: McLloyd Kudzingo
Yemwe akuyimira ngati phungu wachipani cha Malawi Congress (MCP) kudera la Balaka Bwaila, a Andwatch Mambo ati akasankhidwa alimbikira pantchito zotukula maphunziro zomwe akhala akugwira kale kuderali.
A Mambo omwe padakali pano akhazikitsapo kale sukulu za mkomba phala 41 m’madera osiyanasiyana m’bomali, ati apitiriza ntchitoyi ndipo awonetsetsanso kuti sukulu za primary ndi secondary zisamatalikirane kwambiri.
Polankhula pamsonkhano kudera la Group Village M’balasa , a Mambo omwe akhala akugwira ntchito ya uphunzitsi kwa nthawi yayitali, alonjezanso kuti akawasankha, adzaonetsetsa kuti anthu kuderali akupindula ndi ntchito yosiyanasiyana za boma.

Iwo ati anthu kuderali akhala akumanidwa zitukukuko kamba koti anthu omwe akhala akusankhidwa ngati a phungu kuderali, samalabadira kwenikweni za mavuto a anthu.
Pa misonkhano yawo yokopa anthu a Mambo akhala akutsindika kwambiri pa mfundo zotukula maphunziro, umoyo, kutukula achinyamata komanso kuonetsetsa kuti anthu akumwa madzi abwino.
Anthu khumi ndi m’modzi ndiomwe akupikisana pa mpando wa phungu kudera la Balaka Bwaila.