MCP Isesa Mipando Yonse Pa Chisankho Chachibwereza – Mkak

Wolemba: Mtolankhani Wathu


Mlembi wa mkulu wachipani cholamula cha Malawi Congress (MCP) a Eisenhower Mkaka ati ali ndi chikhulupiliro kuti chipanichi chipambana mipando yonse pa chisankho cha chibwereza chomwe chichitike mwezi wa mawa mma dera angapo mdziko muno.

Polankhula lamulungu potsekulira misonkhano yokopa anthu mchipanichi pa sukulu ya pulayimale ya Gwengwere m’boma la Dedza, Mkaka wati a Malawi ambiri padakali pano ndiwokondwa ndi momwe mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera akuyendetsera zinthu mdziko muno.

Polankhulapo, yemwe akuyimira chipani cha MCP pa mpando wa phungu kudera la pakati cha ku m’mawa kwa boma la Dedza a Joshua Malango anati anthu kuderali ayembekezere zitukuko za mnanu zomwe zisinthe kwambiri deralo akasankhidwa kukhala phungu

Bungwe loyendetsa zisankho la MEC likuyembekezeka kuchititsa zisankho za chibwereza m’ma dera ena a phungu komanso ma khansala pa 26 mwenzi wa mawa.

Ena mwa malo omwe bungweli lichititse zisankho ndi dera la ku mpoto cha ku mvuma kwa boma la Nkhota-kota komwe phungu wake adaali malemu Martha Chanjo Lunji achipani chotsutsa cha DPP, pakati cha kumvuma kwa boma la Dedza komwe kudaali phungu wa chipani cholamula cha MCP malemu Mcsteyn Swithin Mkomba kudzanso ku mpoto kwa boma la Mzimba komwe phungu wake a Wezzie Gondwe adatisiya kumayambiliro kwa mwezi uno.

Bungweli lichititsanso zisankho za ma khansala ku Ward ya Chimwalire m’boma la Balaka komwe khansala wake a Josephy Daniel adamwalira pa ngozi ya pa nseu mmiyezi yapitayi.

Potengera ndi momwe zakhala zikuyendera zisankho za chibwereza mmbuyomo, chipani cha MCP ndichomwe chiri ndi mwayi waukulu wopambana pachisankhochi.