HomeHealthAnsah apereka chiyembekezo kwa wodwala khansa, Rose Mzenda

Ansah apereka chiyembekezo kwa wodwala khansa, Rose Mzenda

Wolemba: Mtolankhani Wathu

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Jane Ansah, wapeleka chiyembekezo kwa wodwala khansa, Rose Mzenda, kutsatira kuchitidwa bwino kwa opaleshoni yake, pomutumizira uthenga wolimbikitsa kudzera ku nthumwi za bungwe la Dr.Jane Ansah Foundation.

Nthumwizi zinapita kukaona Mzenda ku Cancer Care Centre Lachisanu pachipatala chachikulu cha Kamuzu Central mu mzinda wa Lilongwe, pa 13 Novembala 2026.

Gulu la bungweli, lomwe linkatsogoleredwa ndi Wotsogolera za Amayi ndi Achinyamata,Lucy Saini, linapita kukakondwerera kupambana kwa opaleshoni yomwe Mzenda anachitidwa Lachinayi, pa 12 Novembala 2026, atakumana ndi mavuto opeza chithandizo cha opaleshoni chomwe ankachifuna mwachangu.

Popereka uthenga wa Wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko linoyu, Saini anati Ansah wakhala akumukumbukira Mzenda m’mapemphero ake kuyambira pomwe anapita kukamuona ku Cancer Care Centre pa 15 Okutobala 2026.

Iye analimbikitsa Mzenda kuti akhale wolimba mtima komanso asataye chiyembekezo pamene akuchira.

“Musataye chiyembekezo chifukwa Mulungu ndiye mchiritsi wa matenda onse. Muli pamaso pa Mulungu, ndipo Wachiwiri kwa Purezidenti sanakuiwaleni chifukwa ndinu mmodzi mwa anthu omwe amawakumbukira m’mapemphero ake,” anatero Saini popereka uthengawo.

Uthengawu unakhudza kwambiri Mzenda, yemwe ankayankha mobwerezabwereza kuti, “Ameni,” posonyeza kuyamikira komanso chikhulupiriro chake.

Saini anafotokoza kuti kupambana kwa opaleshoniyi ndi gawo lofunika kwambiri paulendo wa chithandizo cha Mzenda.

Iye anati nkhaniyi yabweretsa chisangalalo kwa Wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino komanso bungwe la Dr.Jane Ansah Foundation.

Anamulimbikitsanso kuti apitirize kukhala wolimba mtima komanso ndi chiyembekezo pamene akuchira.

Poyankha, Mzenda anayamikira kwambiri Ansah chifukwa chomukumbukira m’mapemphero ake komanso kupitiriza kusonyeza chidwi pa moyo ndi thanzi lake.

Komabe, iye anapempha kuti amuthandize kupeza chikuku choyendera odwala (wheelchair) kuti chizimuthandiza kuyenda pamene akuchira, pofotokoza kuti sanathebe kuyimirira kapena kuyenda yekha kutsatira opaleshoniyo.

Amayi ake komanso omulera, Chimwemwe Mzenda, nawonso anayamikira Wachiwiri kwa wadziko linoyu chifukwa cha chikondi ndi thandizo lake.

Iwo anati akanavutika kwambiri kusamalira mwana wawo popanda thandizo chifukwa cha ukalamba wawo, mavuto azachuma komanso momwe alili ngati mkazi wamasiye.

“Ndikuthokoza Mulungu Wamphamvuyonse chifukwa Wachiwiri kwa Purezidenti amakumbukira anthu osauka kwambiri ngakhale ali ndi ntchito zambiri. Amapezabe nthawi yotithandiza. Mulungu apatse Wachiwiri kwa Purezidenti moyo wautali chifukwa watikumbukira,” anatero Chimwemwe.

Iye anawonjezera kuti amapempherera kuti Mulungu apitirize kudalitsa Ansah komanso gulu la bungweli chifukwa chopita kukaona mwana wake.

Ulendowu ukutsatira ulendo womwe Ansah anachita pa 15 Okutobala 2026, pomwe anakumana ndi odwala khansa ku Cancer Care Centre.

Pa ulendowo, iye anagwiritsa ntchito zomwe anakumana nazo pa moyo wake monga munthu amene anadwalapo khansa n’kuchira polimbikitsa odwala kuti asataye mtima.

Ansah anatsimikiziranso kudzipereka kwake polimbikitsa chiyembekezo, chifundo komanso mgwirizano ndi anthu omwe akulimbana ndi matenda a khansa.

RELATED ARTICLES
- Advertisment -
Google search engine

Most Popular

Recent Comments