Amangidwa kaamba kobela anthu powanamiza kuti awapezera ntchito kuchipatala


Olemba: Sylvester Chibwana

Apolisi ku Lilongwe akusunga mchitokosi amayi awiri ogwira ntchito zachipatala amene akuwaganizira kuti anabera anthu ndalama yokwana K600 000 powanamiza kuti awathandiza kupeza ntchito kuchipatala.

Malingana ndi mneneri wa polisi ya Lilongwe Hastings Chigalu,a Agnes Dzumani omwe amayang’anira odwala pa chipatala cha Bwaila ndi namwino wa pa chiptala cha Kasungu a Ivy Chingumo, akuganiziridwa kuti adachita izi mu February chaka chino.

A Chigalu ati chipatala cha Bwaila chidachititsa mayeso ofuna kulemba anthu ntchito yothandizira ntchito za chipatala (Health Surveillance Assistants), ndipo awiriwa akuti adanyengerera anthu ena atatu kuti apereke ndalama kuti alembedwe ntchitoyi.A Dzumani omwe ndi a zaka 35, akuganiziridwa kuti adauza anthuwa kuti iwo ndiwolemba ntchito pachipatalapa ndipo kuti adapereka nambala ya a Chingumo ponena kuti amenewo ndiwo mkulu wa zaumoyo pa chipatala cha Bwaila.

Akuti anthuwa akawaimbira a Chinguwo omwe ndi a zaka 33, amavomerezadi kuti ndi mkulu wa zaumoyo ndikumawauza anthuwo kuti apereke ndalama kwa a Dzumani ngati akufuna ntchito.

Pakadali pano apolisi ati apezapo K250 000 pa K600 000 yomwe awiriwa anatolera, ndipo oganiziridwawa akaonekera kubwalo la milandu kukayankha mulandu wokuba ponamiza anthu.