Chakwera ndiye adzayimile MCP mu 2025- Ching’oma

By Linda Kwanjana

Mneneli wa chipani cha Malawi Congress (MCP) a Ezekiel Peter Ching’oma,  awuza otsatira chipanichi kuti atakhala pansi ku komiti yaikulu ya chipanichi (NEC) adagwirizana kuti Chakwera ndi amene ataimire chipanichi pamasankho akulu a 2025.

Mukulankhula kwawo ku chinamtindi cha anthu ku Matsimbe Primary School,  a Ching’oma adati Chakwera akuyenera kupitiliza kulamula  kamba koti mu ulamuliro wawo akumana ndi mabvuto ochuluka choncho akuyenera kupitiliza kukonza zinthu.

Pamwambowu, phungu wadelali Francis Berekanyama wapereka mphoto zokwana K6Million kwa osewera mpira  ochita bwino mu Berekanyama Trophy

Kudali kusangalala,  kululutira  pamene phungu wadelaro Francis Berekanyama amapereka mphoto kwa achinyamata mdelalo omwe achita bwino pampikisano wa Berekanyama Trophy.

Mukulankhula kwawo a Berekanyama adayamika achinyamata kamba koonetsa luso pankhani ya zamasewero.

Pamwambowo, Mneneli wa chipani cha Malawi Congress (MCP) a Ezekiel Peter Ching’oma, adayamika a Berekanyama kamba kokhadzikitsa chikho chimenecho.

A Ching’oma adawuza otsatira chipanichi kuti atakhala pansi ku komiti yaikulu ya chipanichi (NEC) adagwirizana kuti Chakwera ndi amene ataimire chipanichi pamasankho akulu a 2025.

Iwo adati Chakwera akuyenera kupitiliza kulamula  kamba koti mu ulamuliro wawo akumana ndi mabvuto ochuluka choncho akuyenera kupitiliza kukonza zinthu.

Mukulankhula kwawo , wapampando wa chipani cha Malawi Congress (MCP) mchigawo cha pakati a Patrick Zebron Chilondola adayamikira mtsogoleri wadziko lino a Lazarus McCarthy Chakwera kamba koti ndi mtsogoleri yekhayo yemwe waonetsa chidwi pankhani zotukula dziko lino. 

Iwo adati pa chifukwachi, a Chilondola apempha a Malawi kuti asagwedezeke.