Mbewe wati wakonzeka kuzathetsa umphawi komanso njala ku Malawi

By Chisomo Phiri

M’modzi mwa omwe awonetsa chidwi chozapikisananawo pa mpando wa mtsogoleri wadziko lino mzisankho za 2025 David Mbewe wati iye msanamira ya mfundo zake yagona pothetsa umphawi komaso njala zomwe zakhala zikuzuza amalawi ochuluka maka akumudzi mdziko muno.

Mbewe yemwe posachedwapa wakhazikitsa chipani chake chotchedwa Liberation for Economic Freedom (LEF) wati iye kukhala mtsogoleri wadziko lino sadzalola kuti m’malawi ndi m’modzi yemwe adzafe ndinjala.

Mwazina iye wati azaonetsetsa kuti amalawi ambiri maka a kumudzi ali ndi mwayi waukulu opeza zipangizo za ulimi pamtengo ozizira.

Prophet Mbewe“Umphawi ndi njala ndizomwe zikupha amalawi ochuluka kunjaku. Nthawi yakwana tsopano kuti David Mbewe apulumutse mtundu wake kumavutowa. Ndili pano kulonjeza kuzathetsa umphawi, njala, nthenda ngakhale sanje pakuti izi zikuzuza mtundu wanga,” anatero Mbewe.

Poyankhapo za SONA yomwe mtsogoleri wadziko lino Lazarus Chakwera anali nayo lachisanu sabata yangothayi, Mbewe wati palibe chachilendo chomwe a Chakwera anena ponena kuti iwo angobwereza zomwe akhala akunena m’mbuyomu ngakhale asanakhale mtsogoleri wadziko lino.

“Mzoseketsa komaso zomvetsa chisoni kuti mtsogoleri alipoyu akungokhala namabweleza zomwe wakhala akulonjeza kwakanthawi koma osakwanilitsa. Izi zikuwapweteka amalawi omwe tsopano maso awo ali pa David Mbewe kuti awapulumutse,” anaonjezera motero Mbewe.

David Mbewe simunthu wachilendo pandale.

Iye wakhalako membala wazipani za DPP komaso UTM.