Wolemba: Mabvuto Kalawa
“Aupeza bambowa tsopano aupeza, amafunafuna pali Yesu tsopano aupeza moyo”- iyi inali nyimbo yomveka lero pamene AMAI a Bungwe la Chikatolika, Catholic Women Association, la Nathenje Parish anali ndi mwambo wa Misa yokumbukira malemu Bambo Francis Damaseke, DP, yemwe anali Bambo Mthandizi pa parishyi.
Mwambo woyamba nthawi ya 9 koloko m’mawa, udatsogoleredwa ndi Bambo Thomas Kasiya, yemwe ndi Bambo Mfumu wa mpingowu komanso mnzake wa ntchito wa malemuyo.
Polankhula poyambitsa mwambowu, Bambo Kasiya adapempha Akhrisitu omwe adafika kuti akhale okonda kupemphera komanso ochita za chifundo, monga momwe malemu Bambo Damaseke ankachitira.
Iye adakumbutsanso Akhrisitu kuti, “Ngakhale papita miyezi iwiri kapena itatu kuchokera pamene Bambo Damaseke anamwalira, misozi idakali m’maso mwathu ndi chisoni. Koma tiyeni tilimbe mtima ndi kupemphera kwambiri, monga momwe malemuyo ankachitira ali moyo. Tiziwapempherera iwo, nawonso azitipempherera. Imfa simathero a moyo. Ndili ndi chikhulupiriro ali m’manja mwa Ambuye,” iwo adatero.

Mawu achilimbikitso a pa mwambowu adachokera m’buku la Mneneri Amosi 9:11-15, ndipo Uthenga Wabwino unawerengedwa m’buku la Maliko.
M’mawu ake, Bambo Kasiya adakumbutsa Akhrisitu za mawu oti _“agape”_ omwe amatanthauza chikondi, ndipo adawalimbikitsa kuti akhale a chikondi monga malemu Bambo Damaseke amene anali wachikondi kwa aliyense.
Pomaliza, banja la a Damaseke lidayamika amayi a Bungwe la Chikatolika chifukwa chokonza mwambowu.
Mayi Patricia Ngozo, yemwe ndi Wapampando wa Bungwe la Amayi, adati adawona kuti n’koyenera kukonza mwambowu chifukwa malemu Bambo Damaseke anali wolimbikitsa kupemphera.
“Ndiyenso amene adapangitsa kuti timbindikiro la Amayi lichitike chaka chatha. Choncho tinagona chanzeru kukumukumbukira m’mapemphero,” iwo adatero. Mayi Ngozo adapemphanso amayi ndi Akhrisitu ena kuti apitirize kupempherera mzimu wa malemu Bambo Damaseke nthawi zonse.
Polankhula ndi olemba nkhani, Mayi Delia Mzoma, yemwe ndi Msungichuma wa mphakati ya Holy Guardian Angels, imodzi mwa mphakati za pa churchyi, adati: “Malemu Bambo Damaseke anali wokonda kupemphera, wachifundo komanso wachikondi.”
Momwemonso, Bambo Laurent Banda, Wapampando wa mphakati ya St. Louis komanso membala wa Bungwe la Chitukuko, adati mpingo unataya munthu wofunika kwambiri.
“Satilekera pa mwambo ngati uwu. Tizipitilizabe kuupanga m’Madera ena chifukwa sanali wansembe wathu yekha. Tizipitiriza kupemphera, chifukwa Bambo Damaseke ankadziwika ndi kulimbikitsa Akhrisitu mu uzimu ndi thupi,” iwo adatero.
Pamwambowu panafika Akhrisitu ndi ana ambiri, ndipo udatsogoleredwa ndi Bambo Mfumu wa parishyi mothandizidwa ndi Abulaza awiri.
Bambo Francis Damaseke anatumikira ngati Bambo Mthandizi kwa zaka 10. Iye anagwiranso ntchito ku St. Patrick’s ndi m’malo ena.
Kuphatikiza pa ntchito ya uparishi, adagwiranso ntchito ku likulu la Mpingo wa Katolika monga wakafukufuku.
Pa nthawi ya mliri wa Covid-19, iye analimbikitsa kupemphera kudzera pa makina a pa intaneti. Ndipo ndi iye amene adayambitsa Bungwe la _“Tiyankhuleni”_ lomwe cholinga chake chinali kupititsa patsogolo kupemphera.
Bambo Francis Damaseke anamwalira mwezi wa April ali ndi zaka 40.
Mzimu wa Bambo Damaseke uupumule m’mtendere.


