Osalowa m’boma ndicholinga chofuna kusolora -Watelo Prophet Mbewe

By Chisomo Phiri

Pomwe kwangotsala miyezi yowelengeka chabe kuti mdziko muno muchitike zisankho zapatatu, mtsogoleri wachipani chatsopano cha Liberation for Economic Freedom (LEF) David Mbewe wapempha onse omwe alindichidwi chopikisananawo pa mpando wa mtsogoleri wadziko lino kuti asakhale ndi maganizo ozalowa m’boma ndicholinga chozazilemeletsa okha kudzera mukatangale.

Mbewe wayankhula izi loweluka mupologalamu ya Times Exclusive.

Prophet Mbewe

Iye anati mzovetsa chisoni kuti anthu ambiri amafuna kulowa m’boma ndicholinga chofuna kubamo mkuzilemeletsa okha pomwe amalawi akuvutika ndi umphawi.

Mbewe anati iye kudzera mchipani chake cha LEF wabwera kuzathetsa mchitidwe ngati uwu.

“Amalawi kunjaku akuvutika. Tiyeni tipewe kulowa m’boma ndicholinga chofuna kubamo mkuzilemeletsa tokha.Ineyo zoti ndingalowe m’boma mkumakaba m’menemo mzosatheka. Mulungu anandidalitsa ndipo ndili ndizondikwanira zomwe sindingafuneso kuba nditalowa m’boma,” anatero Mbewe.

Iye anapitiliza kumema anthu omwe akufuna kolowa chipani chake kuti ali omasuka komaso ololedwa kutelo ponena kuti chipani chake ndi chipani cha m’malawi aliyese.

“LEF sichipani chapamtundu. Ndichipani cha aliyese ndipo nonse muli olandilidwa kulowa chipanichi,” anaonjezera motero Mbewe.