Dr David  Mbewe ati amalawi ataya chikhulupiliro ndi boma


By Chisomo Phiri

Mtsogoleri wachipani cha Liberation for Economic Freedom (LEF) Dr. David Mbewe wadzudzula utsogoleri wa a Lazarus Chakwera ponena kuti ndiomwe ukupangitsa kuti njala isathe mdziko muno kaamba kamfundo zake zopanda masomphenya.

Mbewe amayankhula izi lachinayi pomwe analinawo pa mapemphero¬† Eid-al-Fitr pa mzikiti wa Mangamba m’boma la Machinga.

Mukuyankhula kwake, Mbewe anati kukwela mtengo kwa zipngizo za ulimi komwe a Malawi akukumanako mu utsogoleri wa a Chakwera ndi zina zomwe zikupangitsa kuti njala isathe mdziko muno.


“Anawalonjeza a Malawi kuti azagula feteleza motchipa mpaka K5, 000 thumba koma lero thumba tikumva kuti lili pa K100, 000. Anati azakhazikitsa minda ya ulimi wa mthilira ikuluikulu koma izi sizikutheka chiloweleni m’boma,”anatero Mbewe.

Iye anaonjezeraso kuti umphawi wakula kwambiri mu ulamuliro wa a Chakwera kaamba koti chuma sichikuyendetsedwa bwino zomwe zapangitsa mitengo ya katundu osiyanasiyana kukwera kwambiri.

“Katundu wakwera mitengo koma ndalama sakuyipeza a Malawi. Choncho izi zakolezelaso nkhani ya umphawi mdziko muno. A Malawi alibe chiyembekezo m’boma ili. Boma losaganizira anthu ake,” anaonjezera motere Mbewe.

Iye anapempha asilamu komanso akhilisitu kuti asatope kupempherera dziko lino kuti likwanitse kutuluka m’mavuto omwe likudutsamowa.

M’mawu awo, agulupu Mangamba anati anthu motsogozedwa ndi mafumu ayambe kuopa Mulungu mu zonse, ndipo ati a Malawi aphunzire kupempheleraso atsogoleri kuti zinthu zisinthe.

Imam wanzikiti wa Mangamba, Sheikh Cassim Jenga kudzera muulaliki wake anati asilamu apitilze kupemphera ndi kuchita ntchito zachifundo monga momwe amachitila m’mwezi wa Ramadan.

Pamwambo wa Eid-al-Fitrwu Mbewe anapeleka matumba a simenti komanso anauza asilamu amizikiti itatu kuti akhazikitse magulu kuti awapatse makina opopela madzi paulimi  pofuna kuthana ndivuto lanjala.