Kudwala Kwa Munthu Ndi Chinthu Chomwe Chimagwera Aliyense – Lucius Banda

By Burnett Munthali

Lucius Banda, woyimba wotchuka m’dziko muno yemwenso ndi  mlangizi wa mtsogoleri wa dziko lino pa za luso ndi achinyamata lero wapeleka uthenga kwa owatsatira pa tsamba lawo la mchezo la Facebook kuchokera ku chipatala m’dziko la South Africa komwe anawagoneka chifukwa cha kudwala.

Soldier Lucius Banda

Lucius yemwe amadziwikanso kuti ‘Soldier’ pakati pa anthu okonda nyimbo zake, akudwala ndipo wakhala m’chipatala koposa mwezi tsopano.

Mu uthenga wake wa Facebook, Lucius Banda anapereka moni ndi mawu a chilimbikitso ponena kuti kudwala kwa munthu ndi chinthu chomwe chimagwera aliyense ndipo chofunika ndi kuika chikhulupiriro mwa Yesu.

Anthu osiyana siyana akupitilira kupereka uthenga wa mafuno abwino kutsatira uthenga wakewu.